Tumani
SW

Tumani 歌詞

ジャンルWorld Music
原文言語SW
閲覧数396
Aa表示設定
文字サイズ 18

原文歌詞

SW
翻訳はまだありません。原文を表示しています。
Zikuwoneka ngati anthu oyipa Achuluka kuposa abwino Zikumawonekanso ngati Anthu odziwa malemba Achuluka kuposa owachita Kuno zikumawonekanso ngati Azitumiki anu ambiri Nkhani ya chuma yawayanja Zikumadza wonekanso ngati Uthenga woti mudzabweranso Padakali pano adawupumitsa Ine nde ndimati mwina Mtumeko angelo anu Andipeze mu getsemani Zikuwoneka ngati Mwabwera malonda Mnyumba mwanu Zikuwoneka ngati Pabisala achifwamba Mnyumba mwanu Nde tumani angelo anu Angelo anu Tumani angelo anu Andipeze mugetsemani Zikuwoneka ngati Kwalowa akuba eh eh eh Mnyumba mwanu Zikuwoneka ngati Pabisala achifwamba Mnyumba mwanu Koma zili mnyumba mwanu Yehova mnyumba mwanu Oh mnyumba mwanu Alowetsamo kuba Chigololo komanso malonda ah Mnyumba mwanu Kodi mmesa mumati simusintha Dzulo dzana ndi mkuja Inu muli yemwe uja Mphamvu zanu zili pompaja Mutha kukwapula anthu paja Ngati munachitila kale lija Mkachisi muja Nanga lero bwanji Mtumeko angelo anu Adzawakwapule Tati tumani angelo anu Oh angelo anu Zikuwoneka kuti Anthu atopa ndi bodza Lalowa mnyumba yanu Zikuwonekanso kuti Anthu akulizidwa koma Mnyumba yanu Ine nde ndimati mwina Mtumeko angelo anu Andillimbikitse Tumani angelo anu Andipeze mugetsemani Zikuwoneka ngati Mwabwera malonda Mnyumba mwanu Zikuwoneka kuti Mwalowa chibwana Mnyumba mwanu Nde tumani angelo anu Angelo anu Tumani angelo anu Angelo anu

Namadingo の他の曲

Namadingo →

関連歌詞